Ezekiel 11:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu udandinyamula nukandifikitsa kwa akapolo ku dziko la Babiloni. Zonsezi zidachitika m'masomphenya, monga momwe Mzimu wa Mulungu udaandiwonetsera. Kenaka zinthu zimene ndinkaziwonazo zidayamba kuzimirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera. Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu ku dziko la Akasidi, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandicokera, nakwera.