Ezekiel 11:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake Ambuye Chauta akunena kuti, ‘Mitembo ya anthu ophedwa imene mwaika kumeneko, imeneyo ndiyo nyama. Mzindawu ndiwo mphika ndithu. Koma ndidzakutulutsanimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwake, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzatulutsidwa m'kati mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwace, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzaturutsidwa m'kati mwace.