Ezekiel 12:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu am'dzikomo uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta za anthu okhala ku Yerusalemu ndiponso m'dziko la Israele ndi izi: Anthuwo adzadya buledi mwamantha ndi kumwa madzi mwankhaŵa. Dziko lidzafunkhidwa kwathunthu chifukwa cha nkhondo za anthu onse okhala m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala m'Yerusalemu, ndi za dziko la Israele, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lachipululu, kuleka kudzala kwake chifukwa cha chiwawa cha onse okhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwawuze anthu a mʼdzikomo kuti izi ndi zimene Ambuye Wamphamvuzonse akunena za anthu okhala mu Yerusalemu ndi dziko la Israeli: Iwo adzadya chakudya chawo ndi mantha ndi kumwa madzi awo ndi nkhawa. Zonse za mʼdziko lawo zidzalandidwa chifukwa cha ziwawa za anthu onse okhala mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala m'Yerusalemu, ndi za dziko la Israyeli, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lacipululu, kuleka kudzala kwace cifukwa ca ciwawa ca onse okhalamo.