Ezekiel 12:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukumveka m'dziko la Israelewu ukutanthauza chiyani? Mwambiwo ukuti, ‘Masiku akuchuluka, komabe zolosa sizikuchitika.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israele, wakuti, Masiku achuluka, ndi masomphenya ali onse apita pachabe?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukunenedwa mu Israeli ndi wotani: ‘Masiku akupita koma masomphenya onse sakukwaniritsidwa?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israyeli, wakuti, Masiku acuruka, ndi masomphenya ali onse apita pacabe?