Ezekiel 12:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uŵauze anthu kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndiwuthetsa mwambi umenewu, sudzamvekanso ku Israele. Koma nthaŵi ili pafupi yoti zonse zimene ndidakuululirani m'masomphenya zidzachitikedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzautchulanso mwambi m'Israele; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzachitika masomphenya ali onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho uwawuze anthuwo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndidzawuthetsa mwambi umenewu ndipo sadzawunenanso mu Israeli.’ Uwawuze kuti, ‘masiku ayandikira oti zonse zimene ndinanena mʼmasomphenya zichitikedi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzauchulanso mwambi m'Israyeli; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzacitika masomphenya ali onse.