Ezekiel 12:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo sikudzakhalanso zinthu zina zonama zoziwona ngati kutulo. Sikudzakhalanso kuwombeza koshashalika pakati pa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sikudzakhalanso masomphenya achabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti masiku amenewo sikudzakhalanso masomphenya abodza kapena kuwombeza kwa chinyengo pakati pa anthu a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sikudzakhalanso masomphenya acabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israyeli.