Ezekiel 12:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine Chauta ndidzanena zimene ndidzafune, ndipo zidzachitikadi. Sipakhalanso zochedwa ai, koma masiku anu omwe ano, Ine ndidzalankhula kwa inu anthu aupandunu, ndipo ndidzazichitadi,” ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzacitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwacita, ati Yehova Mulungu.