Ezekiel 12:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, Aisraele akunena kuti zinthu zimene ukuziwona tsopano m'masomphenyazi sizidzachitika konse pa zaka zambiri. Akuti ukulosa zinthu za kutsogolo kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israele akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri; ndipo anenera za nthawi zili kutali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, Aisraeli akunena kuti, ‘masomphenya amene ukuona sadzachitika kwa zaka zambiri. Iwo akuti ukulosa za zinthu zimene zidzachitika ku tsogolo kwambiri.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israyeli akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri: ndipo anenera za nthawi ziri kutali,