Ezekiel 12:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uŵauze kuti, Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso ai. Ndidzachitadi chilichonse chimene ndanena. Ndikutero Ine Chauta!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzacitika, ati Ambuye Yehova.