Ezekiel 12:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Ndipo unyamuke ulendo wako masana ndithu, iwo akuwona, ukachite ngati wopita ku ukapolo kuchoka kwanu kupita ku chilendo, iwowo akuwona. Mwina mwake iwo nkumvetsa ngakhale ali aupandu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nuchoke usana pamaso pao, uchoke pokhala iwepo kunka malo ena pamaso pao; kapena adzachizindikira, angakhale ndiwo nyumba yopanduka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho, iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Unyamuke nthawi yamasana iwo akuona. Uchite ngati wanyamuka kuchoka kumene ukukhala kupita ku dziko lachilendo iwowo akuona. Mwina adzamvetsetsa, paja ndi anthu aupandu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nucoke usana pamaso pao, ucoke pakhala iwepo kumka malo ena pamaso pao; kapena adzacizindikira, angakhalendiwo nyumbayopanduka.