Ezekiel 12:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidachita monga momwe adandiwuzira. Ndidatulutsa katundu wanga masana, nditammanga ngati wopita naye ku ukapolo. Madzulo ndidaboola khoma ndi manja. Pamene chisisira chinkayamba, ndidasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye, iwo akuwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinachita monga momwe anandilamulira, ndinatulutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawatulutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ine ndinachita monga momwe anandilamulira. Nthawi yamasana ndinatulutsa zinthu zanga nditazimanga ngati ndikupita ku ukapolo. Ndipo nthawi yamadzulo ndinabowola khoma ndi manja anga. Pamene chisisira chinkayamba, ndinasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye iwo akuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinacita monga momwe anandilamulira, ndinaturutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawaturutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso: pao.