Ezekiel 13:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndithudi aneneri asokeza anthu anga pomanena kuti, ‘Kudzakhala mtendere,’ pamene kulibe mtendere, ndipo chifukwa anthu akamanga khoma, aneneri amalipaka njereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Popeza kuti aneneri asocheretsa anthu anga pomanena kuti, ‘Kuli mtendere’ pamene mtendere palibe; ndiponso anthu akamanga khoma iwo nʼkumalipaka njereza,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;