Ezekiel 13:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzagwetsa khoma limene mudalipaka njerezalo. Ndidzaligamuliratu mpaka maziko ake ataoneka. Pamene lidzagwa, inunso mudzafera momwemo. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ake agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pake; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzagwetsa khoma limene munalipaka njerezalo. Ndidzaligumuliratu mpaka pansi kotero kuti maziko ake adzaoneka. Khomalo likadzagwa, inu mudzawonongekamo; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ace agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pace; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.