Ezekiel 13:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu zakumutu za anthu a misinkhu yosiyanasiyana, kuti azikola mitima ya anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nkupulumutsa moyo wanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iliyonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu za kumutu za anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nʼkupulumutsa moyo wanu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iri yonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?