Ezekiel 13:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Ndikuzikana zithumwa zanu zapamkono, zimene mumakolera mitima ya anthu ngati mukukola mbalame. Ndidzazithothola pa mikono yanu, kuti ndiŵapulumutse anthuwo amene mumaŵakola ngati mbalame.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kuiuluza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kuiuluza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikudana ndi zithumwa zanu zimene mumakokera nazo mitima ya anthu ngati mbalame. Ndidzazingʼamba kudzichotsa pa mikono yanu. Choncho ndidzapulumutsa miyoyo ya anthu amene munawakola ngati mbalame.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kululuza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kululuza.