Ezekiel 13:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi mabodza anu mudatayitsa mtima anthu anga abwino amene Ine sindidafune kuti ataye mtima. Mudalimbitsa mtima anthu oipa kuti asaleke machimo ao, choncho satha kupulumutsa moyo wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetsa chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza kuti munatayitsa mtima anthu olungama ngakhale sindinafune kuti ataye mtima; ndipo munalimbitsa anthu oyipa kuti asaleka machimo awo motero sakutha kupulumutsa moyo wawo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza mwamvetsa cisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetsa cisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yace yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;