Ezekiel 13:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aneneriwo amalankhula zonama, ndipo amalosa zabodza. Amanena kuti, ‘Akuterotu Chauta,’ pamene Chauta sadaŵatume konse. Komabe amayembekeza kuti zimene anenazo zidzachitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masomphenya awo ndi achabe ndipo kuwombeza kwawo ndi kwabodza. Iwo amati, ‘Yehova akutero,’ pomwe Yehova sanawatume. Komabe iwo amayembekezera kuti zimene ayankhulazo zichitikadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo aona zopanda pace, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatuma, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.