Ezekiel 13:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ine ndikuti, Zimene inu aneneri mukuti mudaziwona m'masomphenya nzabodza. Ndipo kulosa kwanuko nkwabodza. Mumanena kuti ‘Akuterotu Chauta,’ ngakhale Ine sindidalankhule konse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanena?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ine ndikuti masomphenya anu ngachabechabe ndi zimene mwawombedzazo nʼzabodza. Mumanena kuti, ‘Akutero Yehova,’ pamene sindinayankhule nʼkomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Simunaona masomphenya opanda pace kodi? simunanena ula wabodza kodi? pakunena inu, Atero Yehova; cinkana sindinanena?