Ezekiel 13:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukutsutsani chifukwa choti mau anu ngachabe, ndipo zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo nzabodza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndikukutsutsani chifukwa cha zoyankhula zanu zonama ndi masomphenya anu abodzawo. Ndikutero Ine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pace, ndi kuona mabodza, cifukwa cace taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.