Ezekiel 13:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakantha aneneri onama amene amati adaona zakutizakuti ngati kutulo, amenenso kulosa kwao nkwabodza. Sadzakhala nao m'bwalo la aphungu la anthu anga. Sadzalembedwa m'kaundula wa nzika za Israele, ndipo sadzaloŵa m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalanga aneneri amene amanenera zabodza za zinthu zimene amati anaziona mʼmasomphenya. Sadzakhala nawo mʼbwalo la anthu anga ndipo mayina awo sadzalembedwa mu kawundula wa nzika za Israeli. Sadzalowa nawo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pace, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israyeli, kapena kulowa m'dziko la Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova,