Ezekiel 14:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachita zimenezi kuti Aisraele asandithaŵenso, ndipo kuti asiye machimo ao. Pamenepo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti nyumba ya Israele isasocherenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachita zimenezi kuti Aisraeli asasocherenso kundisiya Ine ndi kuti asadziyipitsenso ndi machimo awo. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti nyumba ya Israyeli isasocerenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.