Ezekiel 14:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, dziko likandichimwira, posandikhulupirira Ine, ndidzalikantha ndi dzanja langa ndi kuchepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala m'dzikomo, ndipo ndidzaononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Likandichimwira dziko ndi kuchita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulithyolera mchirikizo wake, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Likandicimwira dziko ndi kucita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulityolera mcirikizo wace, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,