Ezekiel 14:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina ndikadatumiza zilombo kuti ziyende m'dzikomo ndi kuwononga anthu ake, mpaka dzikolo kusanduka chipululu chakuti munthu sangadutsemo chifukwa cha zilombo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikapititsa zilombo zoipa pakati pa dziko, nizipulula ana, kuti likhale lachipululu losapitako munthu chifukwa cha zilombo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikapititsa zirombo zoipa pakati pa dziko, nizipulula ana, kuti likhale lacipululu losapitako munthu cifukwa ca zirombo,