Ezekiel 14:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadatha kupulumutsa ngakhale ana ao omwe. Akadangopulumutsa moyo wao wokha, koma dzikolo likadasanduka chipululu ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lachipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lacipululu.