Ezekiel 14:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadapulumutsa ngakhale ana ao, akadangodzipulumutsa iwo okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chinkana anthu atatuwo akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; koma iwo akadapulumuka okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cinkana anthu atatuwo akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; koma iwo akadapulumuka okha.