Ezekiel 14:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo ngakhale Nowa, Daniele ndi Yobe akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja akadadzipulumutsa iwo okha chifukwa cha kulungama kwao, koma ana ao ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chinkana Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi chilungamo chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cinkana Nowa, Danieli, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi cilungamo cao.