Ezekiel 14:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ena adzatsalako m'dzikomo odzatulutsa ana aamuna ndi aakazi, muŵapenyetsetse akadza kwa inu, muwone m'mene akhalire ndi zimene achite. Mitima yanu idzakhazikika pansi, mukakumbukira zoipa zimene ndachita ku Yerusalemu, chilango chonse chimene ndalanga nacho mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma onani mudzatsala opulumuka m'mwemo amene adzatulutsidwa, ndiwo ana aamuna ndi aakazi; taonani, adzatuluka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zochita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma onani mudzatsala opulumuka m'mwemo amene adzaturutsidwa, ndiwo ana amuna ndi akazi; taonani, adzaturuka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zocita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo.