Ezekiel 14:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitima yanu idzakhaladi pansi, poona m'mene iwo akhalira ndi zimene akuchita, ndipo mudzamvetsa kuti Yerusalemu sindidamchite zimenezi popanda chifukwa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichita kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zocita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazicita kopanda cifukwa zonse ndinazicita momwemo, ati Ambuye Yehova.