Ezekiel 14:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ngati Mwisraele wina aliyense aika mtima pa mafano ake, naikanso maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, kenaka nkupita kwa mneneri, Ineyo Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha moyenerana ndi kuchuluka kwa mafano ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Aliyense wa nyumba ya Israele wakuutsa mafano ake mumtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ake aunyinji;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Ali yense wa nyumba ya Israyeli wakuutsa mafano ace mumtima mwace, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yace pamaso pace, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ace aunyinji;