Ezekiel 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati munthu wina aliyense, Mwisraele kapena mlendo wongokhala nao, andikana Ine, naika mtima pa mafano ake, ndi kuika maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, munthu woteroyo akabwera kudzapempha nzeru kwa Ine, kudzera mwa mneneri, Ine Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera m'Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m'mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ali yense wa nyumba ya Israyeli, kapena wa alendo ogonera m'Israyeli, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ace m'mtima mwace, naimika cokhumudwitsa ca mphulupulu yace pamaso pace, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;