Ezekiel 14:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti ndidzalimbana naye munthu ameneyo. Ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anga. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa chodabwitsa, ndi chizindikiro, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzalimbana naye munthu ameneyo ndipo ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo. Ndidzamuchotsa pakati pa anthu anga. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa codabwitsa, ndi cizindikilo, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.