Ezekiel 15:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ha! Paja ndi nkhuni zosonkhera moto. Tsono moto utapsereza nsonga zake za mtengowo pamodzi ndi mphindikati yake, kodi nkugwira nawonso ntchito ina iliyonse?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zake zonse ziwiri, nupserera pakati pake, kodi ukomera ntchito iliyonse?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, ndi nkhuni chabe zosonkhera moto. Ukaponyedwa pa moto monga nkhuni ndi kuyaka mbali zonse ndi kusanduka makala, kodi ungagwiritsidwe ntchito ina iliyonse?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zace zonse ziwiri, nupserera pakati pace, kodi ukomera nchito Irf yonse?