Ezekiel 15:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndidzaŵalanga. Ngakhale athaŵe moto, motowo udzaŵatenthabe. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵalanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzatuluka kumoto, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawalanga pamenepo ngakhale iwo atuluka pa moto, motowo udzawatenthabe. Ndipo pamene ndidzatsutsana nawo, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzaturuka kumoto, koma moto udzawatha; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.