Ezekiel 16:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato zachikopa. Ndidakupatsa nsalu zabafuta ndi kukuveka zovala zasilika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinakuvekanso ndi nsalu zopikapika, ndi kukuveka nsapato za chikopa cha katumbu; ndinakuzenenga nsalu yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsalu yasilika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato za chikopa. Ndinakuveka zovala zabafuta ndi kukuveka zovala za bafuta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinakubvekanso ndi nsaru zopikapika, ndi kukubveka nsapato za cikopa ca katumbu; ndinakuzenenga nsaru yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsaru yasilika.