Ezekiel 16:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Koma udadzitama nako kukongola kwako ndi kutchuka kwako, ndipo udayamba kuchita zadama. Unkachita chigololo, kumangodzipereka kwa aliyense amene wabwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma unatama kukongola kwako, ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo; unali wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma iwe unatama kukongola kwako ndipo unayamba kuchita zadama chifukwa cha kutchuka kwako. Unkachita chigololo ndi kumangodzipereka kwa aliyense wodutsa ndipo kukongola kwako kunakhala kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma unatama kukongola kwako, ndi kucita zacigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu ali yense wopitapo; unali wace.