Ezekiel 16:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udatenganso zokongoletsera, zopangidwa ndi golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndidakupatsa, ndipo udapangira mafano achimuna amene udachita nawo chigololo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unatenganso zokometsera zako zokoma za golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kuchita nao chigololo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Unatenga zokongoletsera zopangidwa ndi golide ndi siliva zimene ndinakupatsa ndipo unadzipangira wekha mafano aamuna amene unkachita nawo za dama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unatenganso zokometsera zako zokoma za golidi wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kucita nao cigololo.