Ezekiel 16:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udatenga chakudya chimene ndidakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi zimene ndinkakudyetsa, nuzipereka kwa iwo ngati nsembe za fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uchi, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zichite fungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chakudya chimene ndinakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi, zimene ndinkakudyetsa nazo unazitenga nʼkuzipereka kwa mafanowo ngati nsembe ya fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uci, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zicite pfungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.