Ezekiel 16:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakukantha ndi dzanja langa ndipo ndidakuchepetserako dziko lako. Ndidakupereka kwa adani ako, Afilisti, amene ankaipidwa ndi makhalidwe ako onyansa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana akazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ndinatambasula dzanja langa kukukantha ndi kuchepetsa dziko lako. Ndinakupereka kwa adani ako, Afilisti amene amayipidwa ndi makhalidwe ako onyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kucepsa gawo lako la cakudya, ndi kukupereka ku cifuniro ca iwo akudana nawe, kwa ana akazi a Afilisti akucita manyazi ndi njira yako yoipa.