Ezekiel 16:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake udapitirira kuchita chigololo ndi Ababiloni, anthu a m'dziko lokonda lamalonda. Komabe sudakhutire nazo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unachulukitsanso chigololo chako m'dziko la Kanani, mpaka dziko la Ababiloni, koma sunakoledwa nachonso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho unapitirirabe kuchita chigololo ndi Ababuloni, anthu a mʼdziko lokonda zamalonda. Ngakhale unachita izi, komabe sunakhutitsidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unacurukitsanso cigololo cako m'dziko la Kanani, mpaka dziko la Akasidi, koma sunakoledwa naconso.