Ezekiel 16:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye Chauta akunena kuti, “Mtima wako ndi wofooka kwambiri chifukwa udachita zonsezo monga ngati mkazi wadama wopanda manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha? Mtima wako ngwofooka, ati Ambuye Yehova, pakuchita iwe izi zonse, ndizo ntchito za mkazi wachigololo wouma m'maso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ambuye Yehova akuti: Mtima wako ndi wofowoka kwambiri chifukwa unachita zonsezo monga ngati mkazi wopanga manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha! mtima wako ngwofoka, ati Ambuye Yehova, pakucita iwe izi zonse, ndizo nchito za mkazi wacigololo wouma m'maso.