Ezekiel 16:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udamanga nsanja ndi guwa lake pa mseu uliwonse ndiponso kachisi pa bwalo lililonse. Koma iweyo sunkachita monga amachitira adama ena, chifukwa sunkachitira malipiro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakumanga nyumba yako yachimphuli pa mphambano zilizonse, ndi pomanga chiunda chako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Unamanga nsanja pa msewu uliwonse. Unamanganso kachisi pabwalo lililonse. Komabe sunachite ngati mkazi wadama chifukwa unakana malipiro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakumanga nyumba yako yacimphuli pa mphambano ziri zonse, ndi pomanga ciunda cako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.