Ezekiel 16:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amuna amapereka ndalama kwa akazi onse adama. Koma iwe zibwenzi zako zonse unkazipatsa mphatso. Potero unkazinyengerera kuti zizibwera kuchokera mbali zonse kudzagona nawe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu amaninkha akazi onse achigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kuchokera kumbali zonse, kuti achite nawe chigololo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amuna ndiwo amapereka malipiro kwa mkazi wadama. Koma iwe ndi amene ukupereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse. Choncho umazinyengerera kuti zizibwera kwa iwe kuchokera mbali zonse kudzagona nawe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu amaninkha akazi onse acigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kucokera ku mbali zonse, kuti acite nawe cigololo.