Ezekiel 16:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho udaali wosiyana ndi akazi ena pochita zadama, chifukwa panalibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye amene unkapereka ndalama, osati ena kukupatsa ndalama ai. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'chigololo chako; pakuti palibe wokutsata kuchita nawe chigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chotero iwe ukusiyana ndi akazi ena achigololo, pakuti palibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye unkapereka ndalama osati ena kukupatsa ndalama ayi. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'cigololo cako; pakuti palibe wokutsata kucita nawe cigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.