Ezekiel 16:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye Chautawo mau ao ndi aŵa, Udavula mopanda manyazi, udaonetsa maliseche ako pochita zadama ndi zibwenzi zako ndi mafano ako, ndipo udapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zopereka kwa mafanowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nuvundukuka umaliseche wako mwa chigololo chako ndi mabwenzi ako, ndi chifukwa cha mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawapatsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye Yehova akuti, popeza unavula ndi kuonetsa umaliseche wako mopanda manyazi, unachita chigololo ndi zibwenzi zako pamodzi ndi mafano ako onyansa, komanso popeza unapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zoperekedwa kwa mafano,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nubvundukuka umarisece wako mwa cigololo cako ndi mabwenzi ako, ndi cifukwa ca mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawa patsa;