Ezekiel 16:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndidzasonkhanitsa abwenzi ako amene unkasangalala nawo, ndiponso onse amene unkaŵakonda pamodzi ndi onse amene unkadana nawo. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse, nkukuvula pamaso pao, kuti iwowo adzaone thupi lako lonse lamaliseche.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwavundukulira umaliseche wako, kuti aone umaliseche wako wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nʼchifukwa chake Ine ndidzasonkhanitsa zibwenzi zako zonse, zimene unkasangalala nazo, amene unkawakonda ndi amene unkawada. Ndidzawasonkhanitsa motsutsana nawe kuchokera ku madera onse okuzungulira ndipo Ine ndidzakuvula pamaso pawo, ndipo iwo adzaona umaliseche wako wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwabvundukulira umarisece wako, kuti aone umarisece wako wonse.