Ezekiel 16:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakupereka m'manja mwa abwenzi ako. Adzaononga nsanja zako ndi maguwa ako ndi kugwetsa akachisi ako aja. Adzakuvula zovala zako ndi kukukolopola zodzikongoletsera zako zabwinozo. Motero adzakusiya wamaliseche ndi wausiŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yachimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakuvula zovala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakupereka mʼmanja mwa zibwenzi zako ndi kuwononga nyumba zopembedzera mafano ako. Iwo adzakuvula zovala zako ndi kutenga zodzikometsera zako zabwino. Choncho adzakusiya wa maliseche ndi wausiwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yacimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakubvula zobvala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa.