Ezekiel 16:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo utabadwa adakuchita izi: sadadule ntchofu yako, sadakusambitse m'madzi kuti akuyeretse. Sadakuthire mchere monga kudayenera, ndipo sadakukulunge m'nsalu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadule nchofu yako, sanakuyeretse ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthire mchere konse, kapena kukukulunga m'nsalu ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lomwe unabadwa sanadule mchombo wako. Sanakusambitse mʼmadzi kuti uyere. Sanakuthire mchere kapena kukukulunga mʼnsalu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadula ncofu yako, sanakuyeretsa ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthira mcere konse, kapena kukukulunga m'nsaru ai.