Ezekiel 16:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe udaiŵala masiku a ubwana wako, ndipo udandikwiyitsa ndi zinthu zonse zimene udachita. Nchifukwa chake Ine ndidzakubwezera pamutu pako chilango cha zimene udachitazo. Pajatu udaonjezera zigololo pa zonyansa zako zina zonse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza sunakumbukira masiku a ubwana wako, koma wandivuta nazo zonsezi, chifukwa chake taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzachita choipa ichi choonjezerapo pa zonyansa zako zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako koma unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi, Ine ndidzakubwezera ndithu chilango pamutu pako chifukwa cha zimene wachita, akutero Ambuye Yehova. Paja unawonjezera chigololo pa machitidwe ako onyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza sunakumbukila masiku a ubwana wako, koma wandibvuta nazo zonsezi, cifukwa cace taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzacita coipa ici coonjezerapo pa zonyansa zako zonse.