Ezekiel 16:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiwedi mwana wa mai wako amene adadana ndi mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mbale wa abale ako amene adadana ndi amuna ao ndiponso ana ao. Mai wako anali Muhiti, bambo wako anali Mwamori.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe ndiwe mwana wa mai ako wonyansidwa naye mwamuna wake ndi ana ake, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Muhiti, ndi atate wako ndiye Mwamori.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiwedi mwana weniweni wamkazi wa mayi wako, amene amanyoza mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mʼbale weniweni wa abale ako, amene amanyoza amuna awo ndi ana awo. Amayi ako anali Mhiti ndipo abambo ako anali Mwamori.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe ndiwe mwana wa mako wonyansidwa naye mwamuna wace ndi ana ace, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Mhiti, ndi atate wako ndiye M-amori.