Ezekiel 16:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wako ndi Samariya amene ankakhala cha kumpoto kwako pamodzi ndi midzi yake. Mng'ono wako amene ankakhala ndi midzi yake chakumwera kwako, ndi Sodomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala kudzanja lako lamanzere, iye ndi ana ake akazi; ndi mng'ono wako wokhala kudzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ake akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wako anali Samariya, ndipo iye pamodzi ndi ana ake aakazi ankakhala cha kumpoto kwako. Mngʼono wako, Sodomu ankakhala cha kummwera kwako pamodzi ndi ana ake aakazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala ku dzanja lako lamanzere, iye ndi ana ace akazi; ndi mng'ono wako wokhala ku dzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ace akazi.